Paramount Chief Chikulamayembe dies

Lilongwe: Paramount Chief Chikulamayembe of Rumphi died Thursday night at Mzuzu Central Hospital.

Ministry of Local Government and Rural Development Spokesperson Muhlabase Mughogho confirmed the development saying more details about the death and funeral arrangements will be announced later.

In October, 2017, the Tumbuka people held the annual Gonapamhanya festivals that was presided over the chief. Our reporter Kondwani Magombo attended the function and did a story that follows below on the history of the Nkhamanga Kingdom of which he was the king.

The history is written in Chichewa.

Mtundu wa Tumbuka monga mitundu ina yonse, uli ndi mbiri yopatsa chidwi yomwe inachokera patali kwambiri mu ufumu wa Nkhamanga.

Mfumu yaikulu ya Tumbuka ndi Chikulamyembe ndipo malingana ndi kufotokoza kwa mafumu awiri akuluakulu, Mtaziwa ndi Mchinanguwo, a kwa mfumu yaikulu Chikulamayembe ku Bolero, ufumuwu wadutsa muzambiri.

Mfumu yaikulu ya Tumbukayi imatchedwanso Gonapamuhanya ndipo Gonapamuhanya woyamba anali mwana wa Mulowoka Kakalala Sawira yemwe anachokera ku Tanzania ndikuwoloka nyanja ya Malawi kudzera ku Chilumba mchaka cha 1780.

Mulowoka ameneyu anali wa malonda ndipo anabwera pamodzi ndi anthu ena monga Kyungu, Katumbi, Mwahenga, Chipofya, Mwamlowe ndi Kabunduli.

Pamene ena analowera mbali zina, Mulowoka, Chipofya, Mwamlowe ndi Mwahenga anatsika ndi nyanja ndipo Mwamlowe anakhazikika mmbali mwa nyanja komwe aliko mpakana lero.

Mbiri ikuti Mwahenga anakhazikika pa Kabembe ku Mhuju mmbali mwa mtsinje wa Rukuru, pamene Mulowoka ndi Chipofya anakhazikika pa Rumphi. Katumbi anakhazikika pa Kasantha koma patapita nthawi anamwalira.

Mulowoka anapitiliza malonda a mnyanga wa njobvu, nsalu, mikanda, makasu komanso zikopa za nyama monga nkango ndi nyalugwe ndipo anali kuyenda motsika ndi nyanja mpaka ku Dwangwa komwe kumapezeka nyama pa nthawiyo.

Atamva za imfa ya Katumbi anatuma Chipofya ku Kasantha kuti akatenge mbumba ya Katumbi ndikubwera nayo ku Rumphi.

Atabwerera ku Rumphi komwe anamusiya Chipofya Mulowoka anapitilira kupereka makasu komanso nsalu ndi zinthu zina kwa anthundipo pachifukwa cha kukoma mtima kwake anthu anamupatsa mkazi, Nkhulindachi Kumwenda, yemwe anamukwatira ndikubereka mwana, Gonapamuhanya kapena kuti Khalapamuhanya.

Pofuna kubwezera ulemu omwe Mulowoka amachitira anthu powapatsa makasu ndi zinthu zina, anthu anaganiza zosankha Gonapamuhanya kukhala mfumu, akufotokoza motero amfumu a Mtazimva movorezana ndi a Mchinanguwo.

Ichi ndiye chinali chiyambi cha ufumu wa Gonapamuhanya omwe lero lino ndi Chikulamayembe.

Gonapamuhanya anavekedwa ufumu pa malo otchedwa Thulwe koma nkupita kwa nthawi, madzi anayamba kusowa komanso nthaka inali yoguga zomwe zinapangitsa Gonapamuhanya kusamuka ndikukakhazikika pa malo otchedwa Mphande.

Mfumuyi akuti inali ya malamulo okhwima kwambiri ndipo inamanga khoti ndikukhazikitsa malamulo akuti munthu aliyense opezeka ndi mlandu wakupha, uhule kapena ufiti aotchedwe ndi moto.

Koma mng’ono wake wa Gonapamuhanya, Chirambo, anapempha mfumu ya Tumbukayi kuti asinthe chilango popeza kuotcha ndimoto sikunali kwabwino. Mmalo mwake anayamba kugwiritsa ntchito mwavi komabe poona kuti anthu amafabe, anayamba kumamwetsa nkhuku kapena nkhunda za ozengedwa milandu ndipo imene itafeyo mwini wake amapezeka olakwa ndikulipira.

Kuchokera pa Gonapamuhanya woyamba kufikira pa Chikulamayembe yemwe alipo tsopano pakhala mafumu khumi ndi awiri motere: Gonapamuhanya, Chiozga, Bamantha, Bwati, Bwati Puli, Kamphungu, Chakanda, Mkuwayira, Mjuma, Mbauwo Chilongozi, John Ziwange ndi Walter Chenje yemwe alipo tsopano, akutero mafumu awiri a ku Bolerowa .

Ufumu wa Nkhamanga unasefukiranso chakuzambwe mdziko la Zambiya maka panthawi yomwe ankalamulira Chikulamayembe Kamphungu ndipo kufikira lero a Tumbuka amapezeka ku Lwangwa, Muyombe, Chama ndi Lundazi mdziko la Zambia.

Ufumu wa Nkhamanga unakumana ndizokhoma mchaka cha 1881 pamene Angoni anawathira nkhondo ndikuwabalalitsa. Koma zonse zinabwerera mchimake mchaka cha 1907 pamene Mbauwo Chilongozi anakhala pampando wa ufumu.

Malingana ndi kulongosola kwa mafumuwa, Mbauwo Chilongozi anali mtsogoleri wabwino ndipo anamwalira pa 13 August 1931. Mchaka cha 1932 John Zwange anavekedwa ufumu ndipo mchaka chomwechi Walter Chenje anabadwa.

Zwange anali ophunzira kwambiri ndipo anayambitsa kalembera wa anthu omwalira ndi amoyo mu ufumu wa Nkhamanga.

Anasankhanso alangizi omuthandizira monga Katumbi ku Hewe, Salimu Chisovya ku Ng’onga, ndi Chimphapa ku Chiweta.

Iye anakwezanso mafumu monga Mwahenga ku Henga, Mwalweni ndi Kachulu ku Phoka, Mwamlowe ku Mlowe, Mwankhunikira ku Viphya komanso Chapinduka, ku Tcharo.

Zwange anakhazikitsanso lamulo lakuti mwana wina aliyense wa mu ufumu wa Nkhamanga akuyenera kupita ku sukulu.

iye anamwalira mchaka cha 1977 ndipo mwana wake Walter Chenje yemwe anabadwa panthawi yomwe Zwange anavekedwa ufumu analowa ufumu wa Chikulamayembe ndipo alipo kufikira lero ngati mfumu ya nambala 12 kuchokera pa Gonapamuhanya mwana wa Mulowoka Kakalala Sawira.

Pa chifukwa ichi, mfumu Chikulamayembe amadziwika ndi dzina la ulemu lakuti Sawira ndipo udindo wake ndikukweza mafumu, kukhazikitsa zitukuko zosiyanasiyana komanso kuonetsetsa kuti ufumu wa Nkhamanga ndi chikhalidwe cha Tumbuka zikupita patsogolo.

Mchaka cha 2007, mtsogoleri wa dziko lino, malemu Bingu Mutharika anakweza Chikulamayembe kukhala mfumu yaikulu (Paramount Chief).

Likulu la ufumu wa Chikulamayembe liri ku Bolero, m’boma la Rumphi ndipo chaka chilichonse mmwezi wa October kumachitika mwambo otchedwa Gonapamuhanya umene umapereka ulemu kwa mfumu yaikulu yomwe ikulamula.

Mwambo wa Gonapamuhanya umabweretsa poyera chikhalidwe ndi miyambo ya Tumbuka yomwe akhala akutsatira kuyambira kale.

Pamakhala ziwonetsero za zinthu zosiyanasiyana zomwe a Tumbuka ankagwiritsa ntchito kale monga uta ndi mivi (ntcheto) zophera nyama, nsikwa zomwe amasewere pophwetsa mkhuto, komanso zovala zakale zopangidwa kuchokera ku makungwa a mtengo (Nyanda), komanso mowa wa mkontho omwe ndiodziwika Kwambiri pakati pa Tumbuka.

Mwambowu umabweretsanso pamodzi a Tumbuka a ku Malawi ndi a ku Zambia komwe kumachokera mfumu Mphamba, yomwe ndi mfumu yokhayo ya chi Tumbuka ku Zambia.

Cholinga chachikulu cha mwambo wa Gonapamuhanya ndi kudziwitsa mibadwo yalero za mbiri ya Tumbuka, chikhalidwe, miyambo ndi zokonda zawo kuti nawonso apitilire kuuza mibadwo ikubwerayo ndicholinga choti mbiriyi ndi chikhalidwe zisafe, akulongosola motero a Mtaziwa ndi a Mchinanguwo.

Pamwambowu pamakhalanso magule osiyanasiyana omwe atumbuka amavina monga Vimbuza, mbotoska, Mchoma, ndi ena.

Kufikra lero, Atumbuka ndi anthu ogwirizana, olimbikira pa ntchito za chitukuko ndi maphunziro ndipo amapitilira kusunga chikhalidwe ndi miyambo yawo kuyambira kale.

Source: Malawi News Agency MANA